A-Z Lyrics Database
Welcome! Login | Register
Lyrics   »   L   »   Langwan Piksy Lyrics   »   Pakati Lyrics

Langwan Piksy - Pakati Lyrics

Font:      
Align:    
 • VERSE ONE
 • Pakati, pa kuwala ndi mdima
 • Pakati, pakutentha ndi kuzizira
 • Pakati, pa chubu ndi mpira
 • Pakati, pa nkhuku ndi dzira
 • Nkakhala ofunda mudzandilavula
 • Sinfuna kulavulidwa
 • Sinfuna kulavulidwa
 • Ndiri ngati munda wosalambula
 • Ndifuna kupaliridwa
 • Ndifuna kupaliridwa
 • CHORUS
 • Mundiike kumene mufuna
 • Mundiike kumene mufuna
 • Kuti zonse zomwe ndichita
 • Zisangalatse inu
 • Mundiike kumene mufuna
 • Mundiike kumene mufuna
 • Kuti zonse zomwe ndichita
 • Zisangalatse inuyo
 • VERSE TWO
 • Pakati, pa mbuzi ndi gwape
 • Pakati, pa galu ndi nkhadwe
 • Pakati, pa dzulo ndi lero
 • Pakati, pa usiwa ndi ulemelero
 • Nkakhala ofunda mudzandilavula
 • Sinfuna kulavulidwa
 • Sinfuna kulavulidwa
 • Ndiri ngati munda wosalambula
 • Ndifuna kupaliridwa
 • Ndifuna kupaliridwa
 • CHORUS
 • Mundiike kumene mufuna
 • Kumene mufuna
 • Kuti zonse zomwe ndichita
 • Zisangalatse inu
 • Kumene mufuna
 • Mundiike kumene mufuna
 • Kuti zonse zomwe ndichita
 • Zisangalatse inuyo
 • VERSE THREE
 • Sindziwa za mawa
 • Tsono ndikhala ndi nkhawa
 • Ndikhala moyo wa mantha
 • Njira yanga iwunikidwe
 • Odziwa za ku mwamba
 • Akuti ndiri nziwanda
 • Ndikhala moyo wa mantha
 • Ndingatani ndimasulidwe
 • Ndingatani ndimasulidwe
 • Ndiri pa katiiii
 • CHORUS
 • Mundiike kumene mufuna
 • Kumene mufuna
 • Kuti zonse zomwe ndichita
 • Zisangalatse inu
 • Kumene mufuna
 • Mundiike kumene mufuna
 • Kuti zonse zomwe ndichita
 • Zisangalatse inuyo

 • Report error in lyric
  The Pakati lyrics by Langwan Piksy is property of their respective authors, artists and labels and are strictly for non-commercial use only.
  Copyright © 2009-2020 Azlyricdb.com. All Rights Reserved | Privacy policy | Blog
  You are now viewing Langwan Piksy Pakati Lyrics